Mark 6:37 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Yesu adaŵauza kuti, “Inuyo apatseni chakudya.” Iwo adati, “Ndiyetu pafunika kuti tikagule buledi wa ndalama mazana aŵiri kuti tidzaŵadyetse anthu onseŵa!”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma Iye anayankha nati kwa iwo, Apatseni kudya ndinu. Ndipo iwo ananena naye, Kodi tikapita ife ndi kugula mikate ya pa marupiya atheka mazana awiri, ndi kuwapatsa kudya?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma Iye anayankha kuti, “Apatseni kanthu koti adye.” Iwo anati kwa Iye, “Apa pafunika ndalama za miyezi isanu ndi itatu zomwe munthu amalandira! Kodi tipite kukagwiritsa ntchito ndalama zotere kugulira buledi kuti tiwapatse adye?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma Iye anayankha nati kwa iwo, Apatseni kudya ndinu. Ndipo iwo ananena naye, Kodi tikapita ife ndi kugula mikate ya pa marupiya atheka mazana awiri, ndi kuwapatsa kudya?