Mark 6:41 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yesu adatenga buledi msanu uja ndi nsomba ziŵiri zija, nayang'ana kumwamba, nkuthokoza Mulungu. Kenaka atanyemanyema bulediyo, adazipereka kwa ophunzira ake kuti akagaŵire anthuwo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Iye anatenga mikate isanuyo ndi nsomba ziwirizo nayang'ana kumwamba, nadalitsa, nagawa mikate; napatsa kwa ophunzira kuti apereke kwa iwo; ndi nsomba ziwiri anagawira onsewo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Atatenga malofu a buledi asanu ndi nsomba ziwiri, nayangʼana kumwamba, Iye anayamika nagawa malofu a bulediwo. Kenaka anawapatsa ophunzira ake kuti awapatse anthu. Ndipo anagawanso nsomba ziwirizo kwa onse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Iye anatenga mikate isanuyo ndi nsomba ziwirizo nayang'anakumwamba, nadalitsa, nagawa mikate; napatsa kwa ophunzira kuti apereke kwa iwo; ndi nsomba ziwiri anagawira onsewo.