Mark 6:45 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Madzulo omwewo Yesu adalamula ophunzira ake kuti aloŵe m'chombo, atsogole kunka ku tsidya la ku Betsaida, pamene Iye akuuza anthu kuti azipita kwao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pomwepo Iye anakakamiza ophunzira ake alowe m'ngalawa, ndi kumtsogolera kutsidya lija ku Betsaida, m'mene Iye yekha alimkuuza khamulo kuti amuke.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nthawi yomweyo Yesu anawuza ophunzira ake kuti alowe mʼbwato ndi kuti atsogole kupita ku Betisaida, pamene Iye ankawuza anthu kuti azipita.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pomwepo Iye anakangamiza ophunzira ace alowe rri'ngalawa, ndi kumtsogolera kutsidya lija ku Betsaida, m'mene Iye yekha alimkuuza khamulo kuti amuke.