Mark 6:48 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndiye adaona ophunzira aja akuvutika ndi kupalasa chombo, chifukwa anali atayang'anana ndi mphepo. M'mamaŵa kukali mbuu, Yesu adadza kwa iwo, Iye akuyenda pa madzi panyanjapo, nkumafuna kuŵapitirira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pakuwaona ali kuvutidwa ndi kupalasa, pakuti mphepo inadza nikomana nao, pa ulonda wachinai wa usiku Iye anadza kwa iwo, alikuyenda pamwamba pa nyanja; nati awapitirire;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anaona ophunzira ake akuvutika popalasa bwato, chifukwa mphepo imawomba mokumana nawo. Pa nthawi ya mʼbandakucha Iye anafika kwa iwo akuyenda pa nyanja. Anali pafupi kuwapitirira,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pakuwaona ali kubvutidwa ndi kupalasa, pakuti mphepo inadza nikomana nao, pa uionda wacinai wa usiku Iye anadza kwa iwo, alikuyenda pamwamba pa nyanja; nati awapitirire;