Mark 6:56 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kulikonse kumene Yesu ankapita, ku midzi ndi ku mizinda, anthu ankadzakhazika odwala pa mabwalo. Ankamupempha kuti aŵalole odwalawo kungokhudza ngakhale mphonje ya chovala chake. Mwakuti onse amene ankaikhudza, ankachira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kumene konse adalowa Iye m'midzi, kapena m'mizinda, kapena m'milaga, anthu anagoneka odwala pamisika, nampempha Iye kuti akakhudze ngakhale mphonje yokha ya chovala chake; ndipo onse amene anamkhudza anachiritsidwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo kulikonse kumene anapita, ku midzi, mʼmizinda ndi madera a ku midzi, iwo anayika odwala mʼmalo a mʼmisika. Iwo anamupempha kuti awalole kuti akhudze ngakhale mphonje za mkanjo wake, ndipo onse amene anamukhudza anachira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kumene konse adalowa Iye m'midzi, kapena m'mizinda, kapena m'miraga, anthu anagoneka odwala pamisika, 1 nampempha Iye kuti akakhudze ngakhale mphonje yokha ya cobvala cace; ndipo onse amene anamkhudza anaciritsidwa.