Mark 6:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yesu adaitana ophunzira ake khumi ndi aŵiri aja, naŵatuma aŵiriaŵiri. Adaŵapatsa mphamvu zotulutsira mizimu yoipitsa anthu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anadziitanira khumi ndi awiriwo, nayamba kuwatumiza iwo awiriawiri; nawapatsa mphamvu pa mizimu yonyansa;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Atayitana khumi ndi awiriwo, Iye anawatuma awiriawiri ndipo anawapatsa ulamuliro pa mizimu yoyipa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anadziitanira khumi ndi awiriwo, nayamba kuwatumiza Iwo awiri awiri; nawapatsa mphamvu pa mizimu yonyansa;