Mark 7:15 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Palibe chinthu chochokera kunja ndi kuloŵa m'kati mwa munthu chimene chingathe kumuipitsa. Koma zimene zimatuluka mwa munthu ndizo zimamuipitsa.” [
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
kulibe kanthu kunja kwa munthu kukalowa mwa iye, kangathe kumdetsa: koma zinthu zakutuluka mwa munthu, ndizo zakumdetsa munthu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Palibe kanthu kunja kwa munthu kamene kakalowa mwa iye kangamusandutse wodetsedwa. Koma zimene zituluka mwa munthu ndizo zimupanga kukhala wodetsedwa.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
kulibe kanthu kunja kwa munthu kakulowa mwa iye, kangathe kumdetsa: koma zinthu zakuturuka mwa munthu, ndizo zakumdetsa munthu.[