Mark 7:18 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iye adaŵayankha kuti, “Kani ngakhale inunso simumvetsa? Kodi simukudziŵa kuti chilichonse chochokera kunja, ndi kuloŵa mwa munthu, sichingathe kumuipitsa?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ananena nao, Mutero inunso opanda nzeru kodi? Kodi simuzindikira kuti kanthu kalikonse kochokera kunja kukalowa mwa munthu, sikangathe kumdetsa iye;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anawafunsa kuti, “Kodi nanunso simumvetsetsa? Kodi simukuona kuti palibe kanthu kamene kakalowa mwa munthu kochokera kunja kakhoza kumudetsa?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ananena nao, Mutero inunso opanda nzeru kodi? Kodi simuzindikira kuti kanthu kali konse kocokera kunja kakulowa mwa munthu, sikangathe kumdetsa iye;