Mark 7:19 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pajatu sichiloŵa mumtima mwake, koma m'mimba, pambuyo pake nkumakatayidwa ku thengo.” (Pakunena zimenezi, Yesu adagamula kuti zakudya zonse anthu angathe kuzidya.)
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
chifukwa sikalowa mumtima mwake, koma m'mimba mwake, ndipo katulukira kuthengo? Ndipo potero anayeretsa zakudya zonse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakuti sikalowa mu mtima wake koma mʼmimba mwake, ndipo kenaka kamatuluka kunja.” (Ndi mawu amenewa, Yesu anayeretsa zakudya zonse).
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
cifukwa sikalowa mumtima mwace, koma m'mimba mwace, ndipo katurukira kuthengo? Ndipo potero anayeretsa zakudya zonse.