Mark 7:32 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu ena adabwera kwa Iye ndi munthu yemwe anali gonthi ndi wolankhula movutikira. Anthuwo adapempha Yesu kuti amchiritse pomusanjika manja munthuyo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anadza naye kwa Iye munthu wogontha, ndi wachibwibwi; ndipo anampempha Iye kuti aike dzanja pa iye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kumeneko anthu ena anabweretsa kwa Iye munthu amene anali wosamva ndi wosayankhula, ndipo anamupempha kuti asanjike dzanja pa iye.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anadza naye kwa Iye munthu wogontha, ndi wacibwibwi; ndipo anampempha Iye kuti aike dzanja pa iye.