Mark 7:37 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo anthu adazizwa kopitirira ndithu. Adati, “Ameneyu amachita zonse bwino. Ngakhale agonthi amaŵachiritsa nkumamva, ndipo osalankhula amaŵalankhulitsa.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anadabwa kwakukulukulu, nanena, Wachita Iye zonse bwino; angakhale ogontha awamvetsa, ndi osalankhula awalankhulitsa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu anadabwa kwambiri. Iwo anati, “Wachita zonse bwino, ngakhale Iyenso atsekula makutu a osamva ndi osayankhula kuti ayankhule.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anadabwa kwakukurukuru, nanena, Wacita Iye zonse bwino; angakhale ogontha awamvetsa, ndi osalankhula awalankhulitsa.