Mark 7:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Choncho Afarisi ndi aphunzitsi a Malamulo aja adamufunsa Yesu kuti, “Chifukwa chiyani ophunzira anu sasunga mwambo wa makolo, koma amangodya chakudya osasamba m'manja moyenera?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Afarisi ndi alembi anamfunsa Iye, kuti, Bwanji ophunzira anu satsata mwambo wa akulu, koma akudya mkate wao ndi m'manja mwakuda?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho Afarisi ndi aphunzitsi amalamulo anafunsa Yesu kuti, “Nʼchifukwa chiyani ophunzira anu satsatira mwambo wa makolo, mʼmalo mwake amangodya chakudya ndi mʼmanja mwakuda?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Afarisi ndi alembi anamfunsa Iye, kuti, Bwanji ophunzira anu satsata mwambo wa akuru, koma akudya mkate wao ndi m'manja mwakuda?