Mark 8:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsiku lina kudabwera Afarisi ena, nayamba kutsutsana ndi Yesu. Iwo adaapempha Yesu kuti aŵaonetse chizindikiro chozizwitsa chochokera kumwamba. Pakutero ankangofuna kumutchera msampha.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Afarisi anatuluka, nayamba kufunsana naye, ndi kufuna kwa Iye chizindikiro chochokera Kumwamba, namuyesa Iye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Afarisi anabwera nayamba kumufunsa Yesu. Pomuyesa Iye, anamufunsa za chizindikiro chochokera kumwamba.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Afarisi anaturuka, nayamba kufunsana naye, ndi kufuna kwa Iye cizindikilo cocokera Kumwamba, namuyesa Iye.