Mark 8:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yesu adadzumira mu mtima nati, “Kodi bwanji anthu a mbadwo uno amafuna kuwona chizindikiro chozizwitsa? Ndithu ndikunenetsa kuti anthu a mbadwo unowu sadzachiwona chizindikiro akufunacho.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anausitsa moyo m'mzimu wake, nanena, Anthu a mbadwo uno afunafuna chizindikiro bwanji? Indetu ndinena kwa inu, ngati chizindikiro chidzapatsidwa kwa mbadwo uno!
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo anatsitsa moyo nati, “Nʼchifukwa chiyani mʼbado uno ukufuna chizindikiro chodabwitsa? Zoonadi, ndikuwuzani kuti palibe chizindikiro chidzapatsidwa kwa iwo.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anausitsa moyo m'mzimu wace, nanena, Anthu a mbadwo uno afunafuna cizindikilo bwanji? indetu ndinena kwa inu, ngati cizindikilo cidzapatsidwa kwa mbadwo uno!