Mark 8:19 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Muja ndidaanyemanyema buledi msanu kuti ndidyetse anthu zikwi zisanumu, kodi mudaadzaza madengu angati a zotsala?” Ophunzirawo adati, “Madengu khumi ndi aŵiri.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamene ndinawagawira anthu zikwi zisanu mikate isanu ija, munatola madengu angati odzala ndi makombo? Ananena naye, Khumi ndi iwiri.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamene ndinagawa malofu asanu a buledi kwa anthu 5,000, ndi madengu angati amene munatoleramo buledi ndi nsomba zotsalira?” Iwo anayankha kuti, “Khumi ndi awiri.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamene ndinawagawira anthu zikwi zisanu mikate isanu ija, munatola mitanga ingati yodzala ndi makombo? Ananena naye, Khumi ndi iwiri.