Mark 8:23 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yesu adamgwira dzanja, natuluka naye kunja kwa mudzi. Adapaka malovu m'maso mwa munthuyo, namsanjika manja nkumufunsa kuti, “Kodi ukuwona kanthu?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anamgwira dzanja munthu wakhunguyo, natulukira naye kunja kwa mudzi; ndipo atamthira malovu m'maso mwake, naika manja pa iye, anamfunsa, Uona kanthu kodi?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anagwira dzanja la munthu wosaonayo napita naye kunja kwa mudzi. Atalavulira mʼmaso a munthuyo ndi kumusanjika manja, Yesu anafunsa kuti, “Kodi ukuona kalikonse?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anamgwira dzanja munthu wakhunguyo, naturukira naye kunja kwa mudzi; ndipo atamthira malobvu m'maso mwace, naika manja pa iye, anamfunsa, Uona kanthu kodi?