Mark 8:31 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yesu adayamba kuphunzitsa ophunzira ake kuti, “Mwana wa Munthu adzayenera kuzunzidwa kwambiri. Akulu a Ayuda, ndi akulu a ansembe ndi aphunzitsi a Malamulo adzamkana. Iye adzaphedwa, koma patapita masiku atatu adzauka.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anayamba kuwaphunzitsa, kuti kuyenera kuti Mwana wa Munthu akamve zowawa zambiri, nakakanidwe ndi akulu ndi ansembe aakulu, ndi alembi, nakaphedwe, ndipo mkucha wake akauke.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anayamba kuwaphunzitsa kuti, “Mwana wa Munthu ayenera kumva zowawa zambiri ndi kukanidwa ndi akulu a ansembe, ndi aphunzitsi a malamulo, ndi kuti ayenera kuphedwa ndipo patatha masiku atatu adzaukanso.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anayamba kuwaphunzitsa, kuti kuyenera kuti Mwana wa munthu akamve zowawa zambiri, nakakanidwe ndi akuru ndi ansembe akulu, ndi alembi, nakaphedwe, ndipo mkuca wace akauke.