Mark 8:33 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Yesu adacheuka, nayang'ana ophunzira ake ena aja, ndipo adadzudzula Petro. Adati, “Choka apa, iwe Satana! Maganizo akoŵa si maganizo a Mulungu ai, ndi maganizo a anthu chabe.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma Iye anapotoloka, napenya ophunzira ake, namdzudzula Petro, nanena, Choka, pita kumbuyo kwanga, Satana iwe; popeza susamalira zinthu za Mulungu, koma za anthu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma Yesu atatembenuka ndi kuyangʼana ophunzira ake, anamudzudzula Petro nati, “Choka pamaso panga Satana! Suganizira zinthu za Mulungu koma za anthu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma Iye anapotoloka, napenya ophunzira ace, namdzudzula Petro, nanena, Coka, pita kumbuyo kwanga, Satana iwe; popeza susamalira zinthu za Mulungu, koma za anthu.