Mark 8:38 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono ngati munthu achita manyazi ndi Ine ndiponso ndi mau anga pamaso pa anthu ochimwa a makonoŵa amene ali osakhulupirika, ameneyo nanenso Mwana wa Munthune ndidzachita naye manyazi pamene ndidzabwera pamodzi ndi angelo oyera, ndili ndi ulemerero wa Atate anga.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti yense wakuchita manyazi chifukwa cha Ine, ndi cha mau anga mu mbadwo uno wachigololo ndi wochimwa, Mwana wa Munthu adzachitanso manyazi chifukwa cha iyeyu, pamene Iye adzafika nao angelo ake oyera, mu ulemerero wa Atate wake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ngati wina achita manyazi chifukwa cha Ine ndi mawu anga mu mʼbado uno wachigololo ndi wochimwa, Mwana wa Munthu adzachita naye manyazi pamene adzabwera mu ulemerero wa Atate ake pamodzi ndi angelo oyera.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti yense wakucita manyazi cifukwa ca Ine, ndi ca mau anga mu mbadwo uno wacigololo ndi wocimwa, Mwana wa munthu adzacitanso manyazi cifukwa ca iyeyu, pamene Iye adzafika nao angelo ace oyera, mu ulemerero wa Atate wace.