Mark 8:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo Yesu adalamula anthu aja kuti akhale pansi. Kenaka adatenga buledi msanu ndi muŵiri uja, adathokoza Mulungu, namunyemanyema nkumupereka kwa ophunzira ake kuti akagaŵire anthu aja. Ophunzira aja adaŵagaŵiradi anthuwo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo analamulira anthu a khamulo akhale pansi; natenga mikate isanu ndi iwiriyo, nayamika, nanyema, napatsa ophunzira ake, kuti apereke kwa iwo; ndipo anapereka kwa khamulo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anawuza gulu la anthu kuti likhale pansi. Atatenga malofu a buledi asanu ndi awiri, anayamika, nawanyema ndipo anapatsa ophunzira ake kuti agawire anthu, ndipo iwo anatero.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo analamulira anthu a khamulo akhale pansi; natenga mikate isanu ndi iwiriyo, nayamika, nanyema, napatsa ophunzira ace, kuti apereke kwa iwo; ndipo anapereka kwa khamulo.