Mark 9:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamene Yesu ndi ophunzira atatuwo adabwerera kwa ophunzira ena aja, adapeza chikhamu chachikulu cha anthu chitaŵazinga. Aphunzitsi a Malamulo ankatsutsana ndi ophunzirawo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pamene anadza kwa ophunzira, anaona khamu lalikulu la anthu ozungulira iwo, ndi alembi alikufunsana nao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Atafika kwa ophunzira ena aja, anaona gulu lalikulu la anthu litawazungulira ndi aphunzitsi amalamulo akutsutsana nawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pamene anadza kwa ophunzira, anaona khamu lalikuru la anthu ozungulira iwo, ndi alembi alikufunsana nao.