Mark 9:18 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Umati ukangomugwira, umamgwetsa pansi, mwanayo nkumangoti thovu tututu kukamwa, namakukuta mano, mpaka thupi gwagwagwa kuuma. Ndiye ndinapempha ophunzira anuŵa kuti autulutse, koma alephera.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo ponse pamene umgwira, umgwetsa; ndipo achita thovu, nakukuta mano, nanyololoka; ndipo ndinalankhula nao ophunzira anu kuti autulutse; koma sanakhoze.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nthawi iliyonse ukamugwira umamugwetsa pansi. Amatuluka thovu kukamwa, amakukuta mano ake ndipo amawuma. Ndinapempha ophunzira anu kuti awutulutse mzimuwo, koma sanathe.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo ponse pamene umgwira, umgwetsa; ndipo acita thobvu, nakukuta mano, nanyololoka; ndipo ndinalankhula nao ophunzira anu kuti auturutse; koma sanakhoza.