Mark 9:22 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mzimu umenewu wakhala ukumugwetsa kaŵirikaŵiri, mwina amagwa pa moto, mwina m'madzi, kufuna kumupha. Koma ngati Inu mungathe kuchitapo kanthu, chonde tatichitirani chifundo, mutithandize.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kawirikawiri ukamtaya kumoto ndi kumadzi, kumuononga; koma ngati mukhoza kuchita kanthu mtithandize, ndi kutichitira chifundo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
wakhala ukumuponya pa moto kapena mʼmadzi kuti umuphe. Koma ngati mungathe kuchita kanthu, tichitireni chifundo ndipo mutithandize.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kawiri kawiri ukamtaya kumoto ndi kumadzi, kumuononga; koma ngati mukhoza kucita kanthu mtithandize, ndi kuticitira cifundo.