Mark 9:28 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yesu atakaloŵa m'nyumba, ophunzira ake adamufunsa ali paokha, kuti, “Ifeyo ndiye tinalephera bwanji kuutulutsa mzimu woipa uja?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pamene Iye adalowa m'nyumba, ophunzira ake anamfunsa m'tseri, kuti, Nanga bwanji sitinakhoza ife kuutulutsa?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yesu atalowa mʼnyumba, ophunzira ake anamufunsa ali pa okha kuti, “Kodi ndi chifukwa chiyani ife sitinathe kutulutsa chiwandacho?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pamene Iye adalowa m'nyumba, ophunzira ace anamfunsa m'tseri, kuti, Nanga bwanji sitinakhoza ife kuuturutsa?