Mark 9:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zovala zake zidasanduka zoŵala ndi zoyera kuti mbee, kupambana m'mene mmisiri wina aliyense angayeretsere nsalu pansi pano.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo zovala zake zinakhala zonyezimira, zoyera mbu; monga ngati muomba wotsuka nsalu pa dziko lapansi sangathe kuziyeretsai.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Zovala zake zinawala monyezimira kwambiri, kotero kuti palibe sopo wina aliyense amene angaziyeretse monyezimira chotere pa dziko la pansi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo zobvala zace zinakhala zonyezimira, zoyera mbu; monga ngati muomba wotsuka nsaru pa dziko lapansi sangathe kuziyeretsai.