Mark 9:31 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
chifukwa ankaphunzitsa ophunzira ake. Ankaŵauza kuti, “Mwana wa Munthu akudzaperekedwa kwa anthu, ndipo iwowo adzamupha. Koma atamupha, Iye adzauka patapita masiku atatu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti anaphunzitsa ophunzira ake, nanena nao, kuti, Mwana wa Munthu aperekedwa m'manja anthu, ndipo adzamupha Iye; ndipo ataphedwa, adzauka pofika masiku atatu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
chifukwa amaphunzitsa ophunzira ake. Anati kwa iwo, “Mwana wa Munthu adzaperekedwa mʼmanja mwa anthu. Adzamupha, ndipo patatha masiku atatu adzauka.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti anaphunzitsa ophunzira ace, nanena nao, kuti, Mwana wa munthu aperekedwa m'manja a anthu, ndipo adzamupha Iye; ndipo ataphedwa, adzauka pofika masiku atatu.