Mark 9:37 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Aliyense wolandira bwino mwana wonga ngati uyu chifukwa cha Ine, ndiye kuti akulandira bwino Ine amene. Ndipo wondilandira Ine bwino, ndiye kuti akulandira bwino osati Ineyo, koma Atate amene adandituma.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Munthu aliyense adzalandira kamodzi ka tiana totere chifukwa cha dzina langa, alandira Ine; ndipo yense amene akalandira Ine, salandira Ine, koma Iye amene anandituma Ine.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Aliyense wolandira mmodzi wa ana angʼono awa mʼdzina langa alandira Ine; ndipo aliyense wolandira Ine salandira Ine koma amene anandituma.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Munthu ali yense adzalandira kamodzi ka tiana totere cifukwa ca dzina langa, alandira ine; ndipo yense amene akalandira Ine, salandira Ine, koma Iye amene anandituma Ine.