Mark 9:50 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mchere ndi wabwino, koma ngati mcherewo watha mphamvu, mphamvu zakezo nkuzibwezeranso nchiyani? Moyo wanu ukhale ngati wothiridwa mchere, ndipo muzikhala ndi mtendere pakati panu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mchere uli wabwino; koma ngati mchere unasukuluka, mudzaukoleretsa ndi chiyani? Khalani nao mchere mwa inu nokha, ndipo khalani ndi mtendere wina ndi mnzake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Mchere ndi wabwino, koma ngati utasukuluka, mungawukoleretsenso bwanji? Mukhale nawo mchere mwa inu nokha, ndipo mukhale pa mtendere wina ndi mnzake.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mcere uli wabwino; koma ngati mcere unasukuluka, mudzaukoleretsa ndi ciani? Khalani nao mcere mwa inu nokha, ndipo khalani ndi mtendere wina ndi mnzace.