Matthew 1:17 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Choncho panali mibadwo khumi ndi inai kuyambira pa Abrahamu mpaka pa mfumu Davide, mibadwo khumi ndi inai kuyambira pa Davideyo mpaka pa nthaŵi imene Aisraele adaatengedwa ukapolo kupita ku Babiloni, ndiponso mibadwo khumi ndi inai kuyambira pa nthaŵi yotengedwa ukapolo kupita ku Babiloni mpaka pa nthaŵi ya Khristu, Mpulumutsi wolonjezedwa uja.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Motero mibadwo yonse kuyambira pa Abrahamu kufikira kwa Davide ndiyo mibadwo khumi ndi inai; ndi kuyambira pa Davide kufikira pa kutengedwa kunka ku Babiloni mibadwo khumi ndi inai; ndi kuyambira pa kutengedwa kunka ku Babiloni kufikira kwa Khristu mibadwo khumi ndi inai.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kuyambira pa Abrahamu mpaka pa Davide, pali mibado khumi ndi inayi. Ndipo kuyambira pa Davide mpaka pamene Ayuda anatengedwa kupita ku ukapolo ku Babuloni, pali mibado khumi ndi inayi. Ndiponso kuyambira nthawi ya ukapolo ku Babuloni mpaka pamene Khristu anabadwa, palinso mibado khumi ndi inayi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Motero mibadwo yonse kuyambira pa Abrahamu kufikira kwa Davide ndiyo mibadwo khumi ndi inai; ndi kuyambira pa Davide kufikira pa kutengedwa kunka ku Babulo mibadwo khumi ndi inai; ndi kuyambira pa kutengedwa kunka ku Babulo kufikira kwa Kristu mibadwo khumi ndi inai.