Matthew 1:19 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mwamuna wake Yosefe anali munthu wokonda chilungamo, komabe sadafune kumchititsa manyazi poyera. Nchifukwa chake adaganiza za kungothetsa mbeta ija osachitapo mlandu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma Yosefe, mwamuna wake, anali wolungama, ndiponso sanafune kunyazitsa iye, nayesa m'mtima kumleka iye m'tseri.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Popeza Yosefe mwamuna wake anali munthu wolungama, sanafune kumuchititsa manyazi pomuleka poyera. Choncho anaganiza zomuleka mosaonetsera.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma Yosefe, mwamuna wace, anali wolungama, ndiponso sanafuna kunyazitsa iye, nayesa m'mtima kumleka iye m'tseri,