Matthew 1:20 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Akulingalira zimenezi, mngelo wa Ambuye adamuwonekera m'maloto, namuuza kuti, “Yosefe, mwana wa Davide, usaope kumtenga Maria, mkazi wakoyu. Pathupi ali napopa padachitika ndi mphamvu za Mzimu Woyera.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma pakusinkhasinkha iye zinthu izi, onani, mngelo wa Ambuye anaonekera kwa iye m'kulota, nanena, Yosefe, mwana wa Davide, usaope kudzitengera wekha Maria mkazi wako; pakuti icho cholandiridwa mwa iye chili cha Mzimu Woyera.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma akuganiza zimenezi, taonani, mngelo wa Ambuye anamuonekera mʼmaloto nati, “Yosefe mwana wa Davide, usaope kumutenga Mariya kukhala mkazi wako, chifukwa mwana akuyembekezerayo ndi wochokera kwa Mzimu Woyera.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma pakusinkhasinkha iye zinthu izi, onani, mngelo wa Ambuye anaonekera kwa iye m'kulota, nanena, Yosefe, mwana wa Davide, usaope kudzitengera wekha Mariya mkazi wako; pakuti ico colandiridwa mwa iye ciri ca Mzimu Woyera.