Matthew 10:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yesu adasonkhanitsa ophunzira ake khumi ndi aŵiri aja, naŵapatsa mphamvu pa mizimu yoipitsa anthu, kuti aziitulutsa mwa anthuwo, ndiponso mphamvu zochiritsira nthenda zonse za anthu ndi zofooka zao zam'thupi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pamene Iye anadziitanira ophunzira ake khumi ndi awiri, anapatsa iwo mphamvu pa mizimu yoipa, yakuitulutsa, ndi yakuchiza nthenda iliyonse ndi zofooka zonse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yesu anayitana ophunzira ake khumi ndi awiri ndipo anawapatsa ulamuliro otulutsa mizimu yoyipa ndi kuchiritsa nthenda iliyonse ndi zofowoka zilizonse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pamene Iye anadziitanira ophunzira ace khumi ndi awiri, anapatsa iwo mphamvu pa mizimu yoipa, yakuiturutsa, ndi yakuciza nthenda iri yonse ndi zofoka zonse.