Matthew 10:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Munthu aliyense akakana kukulandirani kapena kumvera mau anu, musanse fumbi la kumapazi kwanu potuluka m'nyumbamo kapena m'mudzimo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo yemwe sadzakulandirani inu kapena kusamva mau anu, pamene mulikutuluka m'nyumbayo, kapena m'mudzimo, sansani fumbi m'mapazi anu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ngati wina aliyense sakakulandirani kapena sakamvera mawu anu, musase fumbi la kumapazi anu pamene mutuluka mʼnyumbayo kapena mu mzindawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo yemwe sadzakulandirani inu, kapena kusamva mau anu, pamene mulikuturuka m'nyumbayo, kapena m'mudzimo, sansani pfumbi m'mapazi anu.