Matthew 10:18 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adzapita nanu kwa nduna ndi mafumu chifukwa cha Ine, mwakuti mudzandichitira umboni pamaso pao, ndi pa anthu a mitundu ina.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndiponso adzamuka nanu kwa akazembe ndi mafumu chifukwa cha Ine, kukhala mboni ya kwa iwo, ndi kwa anthu akunja.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chifukwa cha Ine, mudzaperekedwa kwa olamulira ndi kwa mafumu kuti mukhale mboni kwa iwo ndi kwa a mitundu ina.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndiponso adzamuka nanu kwa akazembe ndi mafumu cifukwa ca Ine, kukhala mboni ya kwa iwo, ndi kwa anthu akunja.