Matthew 10:19 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Akadzakutengerani ku milandu, musadzade nkhaŵa nkumanena kuti, ‘Kodi tikakambe bwanji?’ Kapena kuti, ‘Kodi tikanene chiyani?’ Mudzapatsidwa pa nthaŵi imeneyo mau oti munene.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma pamene paliponse angakuperekeni inu, musamadera nkhawa mudzalankhule bwanji kapena mudzanene chiyani; pakuti chimene mudzachilankhula, chidzapatsidwa kwa inu nthawi yomweyo;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma pamene akumangani, inu musadandaule kuti mukanena bwanji kapena mukanena chiyani. Mudzapatsidwa pa nthawi imeneyo zoti munene,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma pamene pali ponse angakuperekeni inu, musamadera nkhawa mudzalankhule bwanji kapena mudzanene ciani; pakuti cimene mudzacilankhula, cidzapatsidwa kwa inu nthawi yomweyo;