Matthew 10:23 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono akamadzakuzunzani ku mudzi wakutiwakuti, mukathaŵire ku mudzi wina. Ndithu ndikunenetsa kuti musanathe kuyendera midzi yonse ya Aisraele, Mwana wa Munthu adzakhala atabwera.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma pamene angakuzunzeni inu m'mudzi uwu, thawirani mwina: indetu ndinena kwa inu, Simudzaitha mizinda ya Israele, kufikira Mwana wa Munthu atadza.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamene akuzunzani pamalo ena thawirani kwina. Pakuti ndikuwuzani zoonadi kuti simudzamaliza mizinda yonse ya Israeli Mwana wa Munthu asanabwere.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma pamene angakuzunzeni inu m'mudzi uwu, thawirani mwina: indetu ndinena kwa inu, Simudzaitha mizinda ya Israyeli, kufikira Mwana wa munthu atadza.