Matthew 10:25 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kumkwanira wophunzira kuti alingane ndi mphunzitsi wake, ndiponso wantchito kuti alingane ndi mbuye wake. Tsono ngati mwini banja anthu adamutcha Belezebulu, nanji a m'banja mwake, kodi sadzaŵatcha maina oipa koposa apa?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kumkwanira wophunzira kuti akhale monga mphunzitsi wake, ndi kapolo monga mbuye. Ngati anamutcha mwini banja Belezebulu, sadzaposa kodi kuwatero apabanja ake?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nʼkoyenera kuti wophunzira akhale ngati mphunzitsi wake, ndi wantchito akhale ngati bwana wake. Ngati mwini banja atchedwa Belezebabu, koposa kotani a mʼnyumba mwake!
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kumkwanira wophunzira kuti akhale monga mphunzitsi wace, ndi kapolo monga mbuye. Ngati anamucha mwini banja Beelzebule, sadzaposa kodi kuwatero apabanja ace?