Matthew 10:29 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Suja amagulitsa atimba aŵiri kandalama kamodzi? Komabe palibe ndi m'modzi yemwe amene angagwe pansi, Atate anu osadziŵa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kodi mpheta ziwiri sizigulidwa kakobiri? Ndipo imodzi ya izo siigwa pansi popanda Atate wanu:
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kodi suja amagulitsa mbalame ziwiri ndi ndalama imodzi? Koma palibe imodzi ya izo imene idzagwa pansi wopanda chifuniro cha Atate anu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kodi mpheta ziwiri sizigulidwa kakobiri? ndipo imodzi ya izo siigwa pansi popanda Atate wanu: