Matthew 10:33 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma aliyense wondikana pamaso pa anthu kuti Ine sandidziŵa, Inenso ndidzamkana pamaso pa Atate anga amene ali Kumwamba kuti sindimdziŵa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma yense amene adzandikana Ine pamaso pa anthu, Inenso ndidzamkana iye pamaso pa Atate wanga wa Kumwamba.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma iye amene andikana Ine pamaso pa anthu, Inenso ndidzamukana pamaso pa Atate anga akumwamba.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma 1 yense amene adzandikana Ine pamaso pa anthu, Inenso nelidzamkana iye pamaso pa Atate wanga wa Kumwamba.