Matthew 10:42 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo aliyense wopatsa ngakhale chikho cha madzi ozizira kwa mmodzi mwa ophunzira angaŵa, chifukwa chakuti ndi wophunzira wanga, ndithu ndikunenetsa kuti ameneyo sadzalephera kulandira mphotho yake.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo amene aliyense adzamwetsa mmodzi wa ang'ono awa chikho chokha cha madzi ozizira, pa dzina la wophunzira, indetu ndinena kwa inu, iye sadzataya mphotho yake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ngati aliyense apereka madzi ozizira a mʼchikho kwa mmodzi wa angʼonoangʼono awa chifukwa cha kuti ndi ophunzira anga, ndikuwuzani zoona, ndithudi sadzataya mphotho yake.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo 10 amenealiyense adzamwetsa mmodzi wa ang'ono awa cikho cokha ca madzi ozizira, pa dzina la wophunzira, indetu ndinena kwa inu, iye sadzataya mphotho yace.