Matthew 11:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kuyambira pa nthaŵi ya Yohane Mbatizi mpaka tsopano anthu akhala akulimbana ndi Ufumu wa Kumwamba, ndipo ochita chamuna ndiwo amene akuulanda.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kuyambira masiku a Yohane Mbatizi, kufikira tsopano lino, Ufumu wa Kumwamba uli wokakamizidwa, ndipo okakamirawo aukwatula ndi mphamvu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kuyambira masiku a Yohane Mʼbatizi mpaka tsopano, ufumu wakumwamba ndi wolimbirana ndipo anthu amphamvu okha ndi amene akuwulanda.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kuyambira masiku a Yohane Mbatizi, kufikira tsopano lino, Ufumu wa Kumwamba uli wokangamizidwa, ndipo okangamirawo aukwatula ndi mphamvu.