Matthew 11:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamene Yohane Mbatizi anali m'ndende, adaamva zimene Khristu uja ankachita. Choncho adatuma ophunzira ake ena kwa Iye kukamufunsa kuti,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma Yohane, pakumva m'nyumba yandende ntchito za Khristu, anatumiza ophunzira ake mau,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yohane ali mʼndende anamva zimene Khristu ankachita, ndipo anatumiza ophunzira ake kukamufunsa Iye.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma Yohane, pakumva m'nyumba yandende nchito za Kristu, anatumiza ophunzira ace mau,