Matthew 11:21 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adati, “Uli ndi tsoka iwe Korazini! Uli ndi tsoka iwe Betsaida! Chifukwa zamphamvu zimene zidachitika mwa inu, achikhala zidaachitikira ku Tiro ndi ku Sidoni, bwenzi anthu ake atavala kale ziguduli nkudzithira phulusa, kuwonetsa kuti atembenukadi mtima.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tsoka kwa iwe, Korazini! Tsoka kwa iwe, Betsaida! Chifukwa ngati zamphamvu zimene zachitidwa mwa inu zikadachitidwa m'Tiro ndi m'Sidoni, akadatembenuka mtima kalekale m'ziguduli ndi m'phulusa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Tsoka kwa iwe Korazini! Tsoka kwa iwe Betisaida! Ngati zodabwitsa zimene zinachitika mwa iwe zikanachitidwa mu Turo ndi Sidoni, iwo akanalapa kale atavala ziguduli ndi kudzola phulusa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tsoka kwa iwe, Korazini! tsoka kwa iwe, Betsaida! cifukwa ngati zamphamvu zimene zacitidwa mwa inu zikadacitidwa m'Turo ndi m'Sidoni, akadatembenuka mtima kale kale m'ziguduli ndi m'phulusa.