Matthew 11:23 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo iwe Kapernao, kodi ukuyesa kuti adzakukweza mpaka Kumwamba? Iyai, adzakutsitsa mpaka ku Malo a anthu akufa. Chifukwa zamphamvu zimene zidachitika mwa iwe, achikhala zidaachitikira m'Sodomu, bwenzi mzindawo ukadalipo mpaka lero.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo iwe, Kapernao, udzakwezedwa kodi kufikira kuthambo? Udzatsika kufikira ku dziko la akufa! Chifukwa ngati zamphamvu zimene zachitidwa mwa iwe zikadachitidwa m'Sodomu, uyo ukadakhala kufikira lero.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo iwe Kaperenawo, kodi udzakwezedwa kufika kumwamba? Ayi, udzatsitsidwa mpaka pansi kufika ku Hade. Ngati zodabwitsa zimene zinachitika mwa iwe, zikanachitika mu Sodomu, bwenzi iye alipo kufikira lero.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo iwe, Kapernao, udzakwezedwa kodi kufikira kuthambo? udzatsika kufikira ku dziko la akufa: cifukwa ngati zamphamvu zimene zacitidwa mwa iwe zikadacitidwa m'Sodomu, uyo ukadakhala kufikira lero.