Matthew 12:22 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambuyo pake anthu adadza kwa Yesu ndi munthu wakhungu, wosatha kulankhula, ndi woloŵedwa mizimu yoipa. Tsono Yesu adamchiritsa, kotero kuti adayamba kulankhula ndi kupenya.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pomwepo anabwera naye kwa Iye munthu wogwidwa ndi chiwanda, wakhungu ndi wosalankhula; ndipo Iye anamchiritsa, kotero kuti wosalankhulayo analankhula, napenya.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pomwepo anthu anabwera naye kwa Yesu munthu wogwidwa ndi chiwanda amene anali wosaona ndi wosamva ndipo Yesu anamuchiritsa kotero kuti atatha anayamba kumva ndi kuona.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pomwepo anabwera naye kwa Iye munthu wogwidwa ndi ciwanda, wakhungu ndi wosalankhula; ndipo Iye anamciritsa, kotero kuti wosalankhulayo analankhula, napenya.