Matthew 12:27 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Inu mukuti Ineyo ndimatulutsa mizimu yoipa ndi mphamvu za Belezebulu, nanga ophunzira anu amaitulutsa ndi mphamvu za yani? Nchifukwa chake ophunzira anu omwewo ndi amene adzakuweruzeni kuti ndinu olakwa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ngati Ine ndimatulutsa ziwanda ndi mphamvu yake ya Belezebulu, ana anu amazitulutsa ndi mphamvu ya yani? Chifukwa chake iwo adzakhala oweruza anu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo ngati Ine nditulutsa ziwanda ndi Belezebule, anthu anu amatulutsa ziwandazo ndi chiyani? Potero tsono adzakhala oweruza anu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ngati Ine ndimaturutsa ziwanda ndi mphamvu yace ya Beelzebule, ana anu amaziturutsa ndi mphamvu ya yani? cifukwa cace iwo adzakhala oweruza anu.