Matthew 12:29 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Palibe munthu amene angathe kuloŵa m'nyumba ya munthu wamphamvu nkufunkha chuma chake, atapanda kuyamba wamumanga munthu wamphamvuyo. Atatero ndiye angafunkhe zam'nyumbamo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kapena akhoza bwanji munthu kulowa m'banja la munthu wolimba, ndi kufunkha akatundu ake, ngati iye sayamba kumanga munthu wolimbayo? Ndipo pamenepo adzafunkha za m'banja lake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Kapenanso wina aliyense angathe bwanji kulowa mʼnyumba ya munthu wamphamvu ndi kunyamulamo zinthu zake, sipokhapo atayamba wamanga munthu wa mphamvuyo? Pamenepo iye akhoza kuba mʼnyumbamo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kapena akhoza bwanji munthu kulowa m'banja la munthu wolimba, ndi kufunkha akatundu ace, ngati iye sayamba kumanga munthu wolimbayo? ndipo pamenepo adzafunkha za m'banja lace.