Matthew 12:32 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chimodzimodzinso aliyense wonenera zoipa Mwana wa Munthu, Mulungu adzamkhululukira. Koma aliyense wonenera zoipa Mzimu Woyera, Mulungu sadzamkhululukira konse nthaŵi ino, ngakhalenso nthaŵi ilikudza.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo amene aliyense anganenere Mwana wa Munthu zoipa, adzakhululukidwa; koma amene aliyense anganenere Mzimu Woyera zoipa sadzakhululukidwa nthawi yino kapena ilinkudzayo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Aliyense amene anena mawu otsutsana ndi Mwana wa Munthu adzakhululukidwa koma aliyense wonena motsutsana ndi Mzimu Woyera sadzakhululukidwa mu mʼbado uno kapena umene ukubwerawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo amene ali yense anganenere Mwana wa munthu zoipa, adzakhululukidwa; koma amene ali yense anganenere Mzimu Woyera zoipa sadzakhululukidwa nthawi yino kapena irinkudzayo.