Matthew 12:36 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndikunenetsa kuti pa tsiku la chiweruzo, anthu adzazengedwa mlandu chifukwa cha mau aliwonse opanda pake amene adaalankhula.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndinena kwa inu, kuti mau onse opanda pake, amene anthu adzalankhula, adzawawerengera mlandu wake tsiku la kuweruza.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ine ndikukuwuzani kuti pa tsiku la chiweruziro munthu adzazengedwa mlandu chifukwa cha mawu aliwonse wopanda pake amene anayankhula.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndinena kwa inu, kuti mau onse opanda pace, amene anthu adzalankhula, adzawawerengera mlandu wace tsiku la kuweruza.