Matthew 12:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Suja adaloŵa m'Nyumba ya Mulungu, nkukadya buledi woperekedwa kwa Mulungu? Chonsecho buledi ameneyo kunali kosaloledwa kuti iyeyo kapena anzakewo nkumudya, koma ansembe okha.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kuti analowa m'nyumba ya Mulungu, nadya mikate yoonetsa, imene yosaloleka kudya iye kapena amene anali naye, koma ansembe okhaokha.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Analowa mʼNyumba ya Mulungu, ndipo iye ndi anzakewo anadya buledi wopatulika amene sikunali kololedwa kwa iwo kudya koma ansembe okha.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
kuti analowa m'nyumba ya Mulungu, nadya mikate yoonetsa, imene yosaloleka kudya iye kapena amene anali naye, koma ansembe okha okha.